Mawu Oyambirira pa Pulojekiti ya Dikeshonale ya Chichewa Print
Cover of the Dictionary

Chida chapadera

Chithunzi chili apa chikusonyeza chikutiro cha chisindikozo chatsopano cha Dikeshonale yathu ya Chichewa/Chinyanja, chimene chinasindikizidwa ku Tchaina posachedwa. Dikeshonaleyi idzapezeka ku sitolo za mabuku ku Afirika ya Chichewa/ Chinyanja kupyolera kwa bungwe la Christian Literature Action in Malawi (CLAIM) ku Ogasiti m’chaka chino cha 2013. Kuposa zisindikizo zapitazo zake bukuli ndi chida chapadera kwa anthu okhala m’madera olankhula Chichewa/Chinyanja a Pakati pa Afirika, makamaka ku Malawi ndi Zambia. Pokhala Dikeshonale yekhayo ya mtundu wake, bukuli ndi chida chofunikira kwambiri kwa anthu a ku Afrika komanso anthu a mitundu ina ogwira ntchito zawo m’maikowa, alendo, ophunzira komanso aphunzitsi, ndinso iwo amene amagwiritsa ntchito Chichewa ndi Chingerezi pogwira ntchito za sayansi kapena maphunziro akachenjede.

Ambiri amene amangagwiritsa ntchito bukuli ali ovutika ndi umphawi wadzaoneni, matenda komanso mavuto odza chifukwa cha kusiyana zikhalidwe. Kusapita patsogolo kwa maphunziro ndi chitukuko zili zina mwa zotsatira za izi, ndipo izi zadzetsa mavuto aakulu. Ogwiritsa ntchito Mtanthauziramawu uyu ali kupatsidwa kuthekera kwa kupyola pa mikwingwirima ya chilankhulo yotere. Pulojekiti yathu ya Mtanthauziramawu ikupenyetsetsa maka pa sukulu ndi malo ena ophunzirira. Tili ndi chiyembekezo kuti tidzatha kupeza chuma choti nkusindikizira mabuku ochuluka zedi a bukuli kuti nkutha kugawa kwaulere kwa ophunzira m’sukulu za sekondare, maka iwo amene ali ana amasiye ndi aphunzitsi awo.

Chichewa/Chinyanja: chilankhulo chofunikira

Map of Malawi

Kuyambira 1997, ine ndakhala ndili kugwira ntchito zanga za Malawi, monga wokhala pamalo komanso bwenzi lochita kuyendera. Ndinaphunzitsa pa Zomba Theological College kwa pafupifupi zaka khumi, ndipo ndinayamba kukhala ndi chidwi chachikulu mu zikhalidwe zina ndi zina za anthu a ku Afirika. Tsopano, pamene tiyang’ana ndi maso apatali kuchokera kuno ku The Netherlands, timagwirabe ntchito zathu ndi dziko la Malawi pamodzi ndi anzanga ena a ku Malawi. Mtanthauziramawu wa Chichewa/Chinyanja ndi ntchito yathu yofunikira.

Chifukwa chiyani timalingaliradi pulojekitiyi? Chilankhulo cha Chingerezi chapezeka kukhala chofunikira kwambiri pakati pa anthu a Pakati ndi Kummwera kwa Afirika. Komabe, zilankhulo za anthu eni ndiye zakhala zida zofunikira kwambiri za kulumikizana pakati pa anthu. Kwa anthu oposa 15 miliyoni a ku Malawi, Zambia, Mozambique, Tanzania, Zimbabwe, Botswana ndiponso South Afrika, Chichewa kapena kuti Chinyanja ndiye chakhala chilankhulo chawo cha tsiku ndi tsiku. Chilankhulo ichi chakhala chikukhala chofunikira ndi champhamvu maka poganizira ntchito za kagwiritsidwe kake pa kulemba ndi kulankhula, ndiponso chifukwa anthu ochuluka a chilankhulawo azindikira ndipo amalimbikitsa kwambiri za mphatso yaikulu ya kulankhula imene iwo ali nayo. Ichi nchifukwa chake chakhala chilankhulo cholumikizitsa anthu onse okhala ku Malawi, ndiponso anthu ochuluka okhala mu madera onse a Pakati ndi Kumwera kwa kontinenti ya Afrika.

Mpungwepungwe wa kumvetsetsana

Panthawi imene ine ndinali kukhala mu Malawi, ndinaona mpungwepungwe waukulu wa kumvetsetsana umene umakhalapo chifukwa cha kusiyana kwa zikhalidwe komanso zilankhulo. Kunena zoona, mpungwepungwe umenewu umakhudza kwambiri magawo onse a kaphunziridwe komanso nkhani za kulumikizanitsa ndi kumvetsetsana pakati pa anthu. Indedi, mu sukulu ndiye mmene vutoli limaonekera koposa madera ena kwambiri. Vuto la kusamvetsetsana pa chilankhulo limakhudza kwambiri anthu osauka, osadziwa kulemba ndi kuwerenga, ana amasiye komanso anthu odwala, popeza izi zimawalepheretsa kuti athe kuyenderana ndi anzawo komanso kuti akhale wa ufulu mu mgwirizano ndi anthu.

Ophunzira a Chichewa ndi Chingerezi anali pa umphawi waukulu pamene kunalibe mabuku a Mtanthauziramawu a mu zilankhulo zawo. Mwamwayi ichi chinasintha chifukwa cha Dikeshonale yathu ya Chichewa/ Chinyanja. Poyamba ine, pothandizidwa ndi anzanga ena, ndinali nawo mwayi wa kutolera mawu ndi kulemba mabuku osiyanasiyana a Mtanthauziramawu a Chingerezi - Chichewa (EC) ndiponso Chichewa – Chingerezi (CE). Madonors ena anandithandiza kuti tithe kusindikiza ndi kufalitsa mabukuwa. Mu kupita kwa nthawi zikwi makumi-makumi za mabuku akhala ali kuperekedwa kwaulere maka kwa ana ophunzira mu sukulu za sekondare. Pofika mwezi wa Febuwale 2009 mabuku awiriwa anali atatha. Ife sitinawasindikizanso.

Tinaganiza zophatikiza mabuku awiri a EC ndi CE kukhala buku limodzi. Mu chaka cha 2009 mbiri ya Mtanthauziramawu wa CE-EC zophatikizidwa inayambika. Mu chaka cha 2010 kusindikiza kwachiwiri kunachitika. Mu Febuwale 2012 kusindikiza kwachitatu kunachitika. Pa nthawi yoyamba dikishonale kunasindikizidwa kunja kwa Malawi. VTR-Publications ku Nürnberg, Jeremane, imapanga ndi kutumiza buku kwa ogwiritsa ntchito lake ku Ulaya, Amereka, ndi malo onse a dziko lapansi, kudzera m’ www.vtr-online.de, Amazon, ndi sitolo zina za mabuku. Dikishonaleyi imapima magalamu 1,300, komanso inakula kwa masamba 884 ndi ndime zoposa 43,000. Chosindikiza chachitatu chilli ndi masamba aakulu, chikutiro chowuma ndi cholimba cha kolite yapamwamba, chimene chimagulika ku dziko lonse lapansi.

Chosindikiza Chachinayi

Mokondwa tikulengeza chosindikiza chachinayi cha dikeshonale ya CE-EC, chimene chinangosindikizidwa ku Tchaina, komanso chimene chidzalowa Afirika ya Chichewa/ Chinyanja mu Ogasiti m’chaka cha 2013. Chosindikizachi chili ndi pafupifupi ndime 45,000, masamba aang’ono 1,152 a pepala yosalemera ya baibulo, komanso chikutiro chowuma ndi cholimba kwambiri, chimene chimakhoza kugwiritsidwa ntchito kwa nthawi zambiri mu nyengo yovuta.

Pulojekiti yathu imadalira opereka ndalama. Mwa njira imeneyo tinakhoza kupereka mabuku kwa ulere kwa ophunzira ndi aphunzitsi ku Malawi ndi Zambia. Moyembekeza zokhudza chosindikiza chachinayi tiyesetsa kuchita ngati kale.

Dikeshonale ya pa Intaneti

Kuonjezera apo, ntchito yotamandika inachitika pamene buku la Mtanthauziramawu wa CE-EC linakhazikitsidwa pa makina a Intaneti, http://translate.chichewadictionary.org pa 28 May chaka cha 2010. Ife tikukhulupilira kuti mabuku a pepala ndi pa makina a intanetiwa adzakhala ali kuthandizirana pokopera anthu amene angakhoza kugwiritsa ntchito dikeshonale komanso kulimbikitsa anthu amene amafuna kwabwino kuti angathandize ntchito imeneyi ndi thandizo la ndalama. Tikupitirizanso ntchito ya kukonza ndi kufufuzafufuza komanso kutolera mawu ena oti nkudzalowetsedwa mu zosindikiza za mtsogolo. Ntchito ya kutukukitsa ndi kukulitsa zamkati mwa buku komanso kutsogolera ntchito ya kusindikiza ndi kufalitsa zimafunikira chidwi chachikulu, maka pa nkhani za ukadaulo wa nzeru, kayendetsedwe koyenera komanso chuma.

Kapezedwe ka chuma cha pulojekiti

Kuchita kafukufuku, kusindikiza mabuku komanso kufalitsa mabuku zimasowekera ndalama zambiri. Kuyambira pachiyambi pa mbiri ya mabuku a Mtanthauziramawu a Chichewa/Chinyanja, mu chaka cha 1854, ntchitoyi yakhala kwambiri ikudalira thandizo la ndalama zochokera ku maiko a kunja, mwachitsanzo Mpingo wa Anglican kudzera mwa ntchito zake za Church Missionary Society, maka mwa bungwe lake la ntchito za mishoni la Universities’ Mission to Central Africa, ndiponso bungwe lake la Society for  Promoting Christian Knowledge, Mpingo wa ku Scotland, komanso wa Free Church of Scotland, African Lakes Company, bungwe la National Education Company of Zambia, gulu la anthu Ogwira ntchito Modzipereka la the US Peace Corps, sukulu ya ukachenjede ya University of South Africa, chipani cha Mpingo wa Katolika cha Fransiscan, komanso Mpingo wa Zambesi Industrial Mission.

Zosindikiza za makono za Mtanthauziramawu wathu zanakhala zakulandira thandizo la chuma kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino, makamaka anthu ndi mabungwe otsatirawa, potsatira ndondomeko ya matchulidwe a maina awo: Burgland, Charitas, Edukans, Evanaid, Koekoek H.M, Koekoek A.A, Liberty, Metgezel, Oikonomos, Protestants Steunfonds, Rotterdam, Share4More, Stephanos, Verheij Consultancy, Weeshuis der Doopsgezinden, Werkgroep Zambia.

Pupils received dictionaries

Polimbikitsidwa ndi nyumba zobukitsa ndi kufalitsa mabuku komanso sitolo zogulitsa mabuku, msika waung’ono wogulitsa madikeshonale unakhazikitsidwa mu madera a Afirika ya Chichewa/Chinyanja. Kugulitsa mabuku a Mtanthauziramawu kwathandiza kupeza ndalama, koma izi mpang’ono chabe. Tikukhulupilira kuti ndondomeko yabwino ya kagulitsidwe ka mabukuwa idzapitirira ndi kulimbikitsidwa ndi chitukuko chimene chikubwera cha maphunziro komanso pa chuma. Gulu la anthu limakula limene limatha kugula mabukuwa kudzera mu sitolo zogulitsira mabuku za ku Malawi ndi Zambia. Komatu anthu ochuluka zedi sanayambepo alowa ndi kuona kuti mkati mwa sitolo yogulitsira mabuku mumaoneka motani. Chikhalirecho ambiri a iwowa ndi achichepere, maka ophunzira m’sukulu zosiyanasiyana. Iwo akufunikiradi Mtanthauziramawu uyu. Tikuyembekeza kuti mabungwe ambiri omwe samayendetsedwa ndi boma (NGOs), maofesi a boma, sukulu zambiri, mipingo komanso mabungwe ndi magulu osiyanasiyana adzakhala ali kugulira mabukuwa kwa antchito awo, ophunzira kapenanso mamembala awo. Pa buku lililonse limene iwo angagule, ife tikhoza kulipirapo buku limodzi kwa mwana wasukulu wa ku Malawi kapena wa ku Zambia amene sangathe kudzigulira mwa iye yekha.

Kufikira tsopano, mbiri ya kapangidwe ka madikeshonale a Chichewa yakhala yodalira kwambiri pa thandizo la maiko akunja. Koma ife tili ndi chikhulupiriro kuti atsogoleri a ntchito za maphunziro a maiko olankhula Chichewa/Chinyanja akukulitsa kufunikira kwake kwa kuzindikira udindo wawo pa mabuku a chinenero. Zitsanzo zabwino ndi mmene limagwirira ntchito zake ndi bungwe la Centre for Language Studies (CLS) la University of Malawi ku Zomba komanso Malawi Institute of Education (MIE) ku Domasi. Iwo akuzindikira kufunikira kwa kuyikirapo mtima kwa anthu a mu Afirika pa ntchito ya kutolera ndi kulemba madikeshonale. Pa nthawi yomweyo Afirika isachite manyazi pamene m’ntchito iyi imathandizidwa ndi opereka ndalama komanso akatswiri za zilankhulo. Anthu onse ali olumikizana ngati anthu a mudzi umodzi wa dziko lapansi, anthu a ku Mpoto ndi anthu a Kummwera akuyenera kugwirira ntchito zawo limodzi kuti ziwathandize onse limodzi. Mabuku a Mtanthauziramawu ali kugwira ntchito ya kukwirira phompho la kusalankhulana.

Kupempha chithandizo

Pomwe inu mungathandize Pulojekiti imeneyi, ndiye kuti mudzakhala mukutengapo gawo la kuthana ndi mavuto a za maphunziro mu madera olankhula Chichewa/ Chinyanja a mu Afirika. Mtanthauziramawu amachepetsa kusamvetsetsana kumene kungakhalepo pakati pa anthu olankhula Chingerezi ndi olankhula Chichewa/Chinyanja. Chonde zindikirani kuti Pulojekitiyi simaphatikizapo ndalama zofunikira potolera ndi kulemba mawu, kukonza ndi kusanja kwa buku ngakhalenso buku la pa makina a Intaneti, popeza ntchito zimenezi zakhala zimachitidwa kwaulere, poganizira ndi kuthandiza anthu a ku Afirika.

Muthandize mwa njira zotere:
-Gulani madikeshonale ku VTR-Publications (lembani: Chichewa).
-Kwa anthu a ku Afirika ya Chichewa/ Chinyanja: gulani madikeshonale ku sitolo za mabuku  ku Malawi, Zambia, ndi zina zotero; sitolo zichite oda kwa CLAIM ku Blantyre, This e-mail address is being protected from spambots. You need JavaScript enabled to view it  
-Ngati inu sindinu sitolo, gulani madikeshonale ochuluka a mtengo wotsitsidwa ku Foundation Heart for Malawi, This e-mail address is being protected from spambots. You need JavaScript enabled to view it
-Perekani mphatso za ndalama, tabwanyani batani lolemba ‘How to Contribute

 
Providing a tool for communication in Chichewa/ Chinyanja speaking Africa   Webmaster -  Copyright © 2016 Steven Paas